Typ-hier-de-titel

The Way To God
                 CHICHEWA
                            .MALAWI  ….malawi…..                    

NJIRA YA KWA MULUNGU

Koma iye analasidwa chifukwa cha zolakwa zatu, natundudzidwa chifukwa cha mphullupulu zathu;
chilango chotitengera ife mtendere chinamgwera iye, ndipo ndi mikwingwirima, ndipo ndi mikwingwirima yache ife tachiritsidwa.  Yesaya 53:5
MULUNNGU AKUTI:
LERO ngati mudzamva mau ache, musaumitse mitima yanu.  Ahebr 4:7

CHIYANJANO
Koma onse amene anamulandila iye, (Yesu) kwa iwo anapatsa mphamvu yakukhala ana a Mulungu, kwa iwotu, akukhulupilira dzina lache.  Yohane 1:12

KUOMBOLEDWA
Ndipo mwa iye tiri ndi maomboledwe mwa mwazi wache, chikhululukiro cha zochimwa zanu.  Aefeso 1:7

CHIPULUMUTSO
Iye amene akukhulupilira mwana’yo ali nao moyo wosatha.  Yohane 3:16, 36

IMFA YA YESU
Chifukwa chache, inali yofunika kupatsa anthu ochimwa mtendere ndi Mulungu. “Chifukwa cha imfa ya Khristu Ya pa mtanda yapanga mtendere ndi Mulungu kwa ONSE kupyolera m’mwazi wacha”.  Akolose 1:20

YESU YEKHA MWANA WA MULUNGU
Angathe kupulumutsa inu ndi ine, palibe munthu ndipo palibe chiri chonse chingathe podziwa kuti: “…..Simunaomboledwa ndi zovunda, golidi ndi Silva, …Koma ndi mwazi wache wamtengo wapatali wa Khristu.”  1.Petro 1:18, 19

YESU AMAYERETSA
Onse amene ali osayeretsedwa, Inunso, muli osayera, chache chifukwa “Ndani anganene, Ndasambitsa mtima wanga, ndayera opanda tchimo?”  Miyambo 20:9

Inu, amene mukufuna kupulumutsidwa ndi kuyeretsedwa, Mulugu sakupemphani kuchita chiri chonse koma kubvomereza zolakwa zanu ndi kukhulupilira kuti mwazi wa Yesu, umene unakhetsedwa pa mtanda wa Gologota chifukwa cha inu, kuti mupulumsidwe chanu.

“Ndipo mwazi wa Yesu, mwana wa Mulugu, Utisambitsa kutichotsera uchimo wonse.”  1.Yohane 1:7

“Ngakhale zoipa zanu zili zofiira, zidzayera ngati matalala.”  Yesaya 1:8, Masalmo 51:7

Tsopano ndi nthawi yabwino kwa iwe, ilipo nthawi yachisomo kwa iwe, mawa mungachedwe kwambiri. Sitikuuzani izi Pokuopsyetsani ayi, koma chifukwa cha ambiri anakutsogolerani opanda kusannkha Yesu, pomwe iwo anadziwa zomwe anawakonzera. “iye amene sakhulupilira adzalangidwa.”  Marko 16:16

Ambiri amene anasankha moyo wa mtendere, moyo wosatha, moyo ndi Yesu, anaziwa kutii Bukhu lopatulika mpaka lero, ngati lingatengedwe kukhala loyera monga Mau a Mulungu.

Iwo angathe luchitira umboni zimene Yesu wa achitira. Ngakhale ife titha kukhala mboni kupyolera mwa Mzimu wa Mulungu, kuti Yesu ndi wamoyo, akupulumusa ndi kuchiritsa.

Yesu anatinso:
Ine ndine kuuka ndi Moyo; lye amene Akhulupirira, angakhale amwalira, adzakhala ndi moyo (Yohane Woyera 11:25). Kodi inu mukhullupilira izi?

Funso ili linafunsidwa kwa mkazi mu Israël ndipo iye akufunsa INU LERO
kodi mukukhulupilira kuti kupyolera mukukhulupilira mwa Yesu, tingathe kulandila mtendere ndi Mulungu? Bukhu Lopatulika likuti, munthu angathe kuchoka M’moyo wa imfa mu tchimo ndi kulowa mu moyo osatha ndi Yesu Khristu ngati munthu abadwanso.
Uthenga wabwino woyenera kuukhulupilira!

TICHITE CHIYANI TSOPANO!
Bvomereza kuti ndiwe wochimwa pamaso pa Mulungu ndi kukhala ndi chikhulupiliro mwa Yeso, amene adzakhululukira iwe, bvomereza machimo ako pamaso pa Mulungu. Muuzeni iye mum au anu (Kupemphera ndiko kulankhula ndi Mulunga) zonse zimene ziri kukubvutani inu ndipo mukhulupilire kuti Yesu adzakhululukira machimo anu TSOPANO!
Werengani bakhu Lopatulika tsiku ndi tsiku. Yambani, kuyankhula, ndi Yohane Woyera.

Ngati mukufuna kulandira mathalaki ndi timabuku tauthenga wabwino kapena kumva zambiri (kwa ulere) lemberani ku Keyela ili músiyi.